Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Luka 24:11 - Buku Lopatulika Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam'kutu, mwakuti sadaŵakhulupirire azimaiwo. [ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. |
Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.
Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!
Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?
Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwe kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.