mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.
Luka 24:10 - Buku Lopatulika Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohana, ndi Maria, amake a Yakobe. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. |
mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.
Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.
nabwera kuchokera kumanda, nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe.