Luka 23:9 - Buku Lopatulika Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Herode adamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sadamuyankhe kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe. |
Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.
Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.
Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegule pakamwa pake.
amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;