Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.
Luka 23:6 - Buku Lopatulika Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Pilato adamva zimenezi, adaŵafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndi wa ku Galileya?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya. |
Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.
Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.
Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.
Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa.
Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.