Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.
Luka 23:3 - Buku Lopatulika Ndipo Pilato anamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye anamyankha nati, Mwatero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Pilato anamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye anamyankha nati, Mwatero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pilato adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.” |
Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.
Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.
Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo Iye anati kwa iwo, Munena kuti ndine.
Chifukwa chake Pilato anatulukira kunja kwa iwo, nati, Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?
Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato;