Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
Luka 23:16 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.” [ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.” |
Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda.
Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.
Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeze chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.
Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.