Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba.
Luka 23:12 - Buku Lopatulika Ndipo Herode ndi Pilato anachitana chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Herode ndi Pilato anachitana chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato adayamba kuyanjana, chonsecho kale ankadana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani. |
Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba.
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;