Luka 23:10 - Buku Lopatulika Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anaimirira, namnenera Iye kolimba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anaimirira, namnenera Iye kolimba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaimirira pomwepo nkumaneneza Yesu kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri. |
Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri;
Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.
Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.
Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.
Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;