Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake.
Luka 22:7 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku la buledi wosafufumitsa lidafika, ndiye kuti tsiku limene anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe. |
Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake.
Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.
Ndipo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa chinayandikira, ndicho chotchedwa Paska.
Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.
Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;