Luka 22:6 - Buku Lopatulika Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yudasi adavomera, nayamba kufunafuna mpata woti amuperekere kwa iwo, anthu onse osadziŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi. |
Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska.