Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.
Luka 22:57 - Buku Lopatulika Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Petro adakana, adati, “Mai iwe, sindimdziŵa ameneyu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.” |
Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.
Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye.
Ndipo popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine.
Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.
Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.