Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.
Luka 22:5 - Buku Lopatulika Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adakondwa, nalonjeza kumpatsa ndalama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. |
Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.
Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.
(Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;
Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.
posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;
Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.
Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.