Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.
Luka 22:34 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ndikukuuza, iwe Petro, kuti lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.” |
Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.
Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.
Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.
Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.
Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.
Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.