Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.
Luka 22:16 - Buku Lopatulika pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti kunena zoona, sindidzadyanso konse Paska, mpaka Paskayi itadzafika pake penipeni mu Ufumu wa Mulungu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.” |
Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.
Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.
Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paska uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa;
pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.
Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.