Luka 22:13 - Buku Lopatulika Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono iwo adapita nakachipezadi monga momwe adaaŵauzira, ndipo adakonza phwando la Paska. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska. |
Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko.
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.