Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga?
Luka 22:12 - Buku Lopatulika Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.” |
Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga?
ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.
Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.
Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.