Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.
Luka 22:11 - Buku Lopatulika Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda chimene Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’ |
Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.
ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m'menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga?
Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mzinda, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.
Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko.
Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.
Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.