si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.
Luka 22:10 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mzinda, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Mvetsani! Mukangoloŵa m'mudzimu, mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire mpaka kunyumba kumene akaloŵe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe, |
si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.
Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga?
Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.