Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
Luka 21:8 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Chenjerani kuti anthu angakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Azidzatinso, ‘Nthaŵi yayandikira.’ Amenewo musadzaŵatsate. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo. |
Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike?
Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.
Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.
Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.
Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.
Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.
Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.