Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 21:7 - Buku Lopatulika

Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu aja adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”

Onani mutuwo



Luka 21:7
13 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?


Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?


Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?


Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:


Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika.


Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pamwala unzake, umene sudzagwetsedwa.


Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.