Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu wa Ziyoni.
Luka 21:22 - Buku Lopatulika Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa. |
Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu wa Ziyoni.
ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;
Pakuti tsiku lakubwezera lili mumtima mwanga, ndi chaka cha kuombola anthu anga chafika.
Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.
Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.
Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;
koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.