Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe. Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?
Luka 21:11 - Buku Lopatulika ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba. |
Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe. Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?
Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi chivomezi, ndi mkokomo waukulu, kamvulumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.
Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo.
Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.
Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina:
Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.