Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?
Luka 20:9 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wampesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Yesu adaphera anthu aja fanizo lina. Adati, “Munthu wina adaalima munda wamphesa. Adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina, nakakhalako nthaŵi yaitali. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali. |
Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?
Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.
Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.
Ndipo Yesu anati kwa iwo Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu izi.
Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.