kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!
Luka 20:47 - Buku Lopatulika amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero aatali; amenewo adzalandira kulanga koposa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.” |
kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!
Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.
ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;
Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.
Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.
Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.
Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.
Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;
Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.
Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.