pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.
Luka 20:41 - Buku Lopatulika Koma Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye mwana wa Davide? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye mwana wa Davide? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, bwanji amati Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide? |
pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.
Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.
Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?
Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;
Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi mu Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.