Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.
Luka 20:11 - Buku Lopatulika Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatumanso wantchito wina. Nayenso alimi aja adammenya, namchita chipongwe, nkumubweza osampatsa kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu. |
Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.
Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi.
Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.
Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;
koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.