Luka 2:47 - Buku Lopatulika Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. |
Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:
Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?
Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.
Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?