Luka 2:42 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. |
ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe;
Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.
Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.