Luka 2:40 - Buku Lopatulika Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye. |
Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.
Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.
Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta.
Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.