Luka 2:30 - Buku Lopatulika chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu, |
Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.
inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.