Luka 2:29 - Buku Lopatulika Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza, tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere. |
Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo.
Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.
Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye.
Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.
ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?