Ndipo ndinatenga kalata yogulira, yina yosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi yina yovundukuka;
Luka 2:27 - Buku Lopatulika Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adaloŵanso m'Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, |
Ndipo ndinatenga kalata yogulira, yina yosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi yina yovundukuka;
Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye,
Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.
Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu
Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.
Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;
pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleze;
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,
Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.