A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.
Luka 2:21 - Buku Lopatulika Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe. |
A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.
Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.
Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.
ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.