Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Luka 2:19 - Buku Lopatulika Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira. |
Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.
Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga.
Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.
Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.
Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.