Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.
Luka 2:17 - Buku Lopatulika Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adamuwona, abusawo adaŵafotokozera zimene mngelo uja adaaŵauza za mwanayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo, |
Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.
Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.
Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.
Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.
Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumzinda wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.