Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Luka 2:16 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m'chodyera cha zoŵeta chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe. |
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda;
Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera.
Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife.
Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.