Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Luka 19:5 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” |
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m'mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.
Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma.
Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi.
Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,
kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,
Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.