Luka 19:41 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene anayandikira, anaona mudziwo naulirira, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira |
Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.
Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.
Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.
Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumire kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumbe tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu.
Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!
Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.
nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.