Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;
Luka 19:11 - Buku Lopatulika Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ankamva zimene Yesu ankalankhula. Tsono adaŵaphera fanizo, popeza kuti anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo ankaganiza kuti Mulungu akhazikitsa ufumu wake posachedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. |
Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;
Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,
Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi ino mubwezera ufumu kwa Israele?