Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
Luka 19:10 - Buku Lopatulika Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.” |
Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israele.
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.
Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza?
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.