Luka 18:34 - Buku Lopatulika Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula. |
Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!
Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.
Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.