Luka 18:2 - Buku Lopatulika nanena, M'mzinda mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena, M'mudzi mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adati, “M'mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu. |
Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asiriya wathyola chipangano, wanyoza mizinda, sasamalira anthu.
Ndipo m'mzinda momwemo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane.
Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu;
Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzachita chiyani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamchitira iye ulemu.
Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?