Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa?
Luka 17:7 - Buku Lopatulika Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adatinso, “Utha kukhala ndi wantchito wolima ku munda kapena woŵeta nkhosa. Pamene iye wafika kuchokera ku munda, kodi ungamuuze kuti, ‘Bwera msanga, udzadye?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’ |
Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa?
Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng'ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?
Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.
wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?