Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.
Luka 17:5 - Buku Lopatulika Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atumwi adapempha Ambuye kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!” |
Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.
Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.
Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.
Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.