Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Luka 17:22 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Akudza masiku pamene mudzalakalaka kuwona nthaŵi ya kudza kwa Mwana wa Munthu ngakhale tsiku limodzi lokha, koma simudzaloledwa ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake, “Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. |
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo.
Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.
Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.
Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.
Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.