Luka 17:18 - Buku Lopatulika Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeke mmodzi kodi, koma mlendo uyu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye kuti sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?” |
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.
koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.