Luka 17:16 - Buku Lopatulika ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo anali Msamariya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya. |
Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.
Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse.
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.
Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).
kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.
Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.
zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.
Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.
akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,