Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Luka 17:13 - Buku Lopatulika ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nanena mokweza mau kuti, “Yesu Ambuye, tichitireni chifundo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!” |
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.
Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.
Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m'kumuka kwao, anakonzedwa.
Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.