Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.
Luka 17:12 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene analowa Iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene analowa Iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ankaloŵa m'mudzi wina, anthu khumi akhate adadzamchingamira. Adaima kutali, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali |
Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.
Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?
Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.
Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.