Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 16:7 - Buku Lopatulika

Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata yako nulembere makumi asanu ndi atatu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adafunsanso wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yotani?’ Iye adati, ‘Tirigu wamuyeso wokwanira matumba makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, ungolembapo matumba makumi asanu ndi atatu.’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’ “Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000. “Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’

Onani mutuwo



Luka 16:7
7 Mawu Ofanana  

Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.


Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata yako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.


Ndipo anatumizanso wina wachitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja.


Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wampesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu.